60 ndi ku pfuko la Benjamini Geba ndi mabusa ace, ndi Alemeti ndi mabusa ace, ndi Anatoti ndi mabusa ace. Midzi yao yonse mwa mabanja ao ndiyo midzi khumi ndi itatu.
61 Ndipo otsala a ana a Kohati analandira mwa maere, motapa pa mabanja a pfuko, pa pfuko la Manase logawika pakati, midzi khumi.
62 Ndi kwa ana a Gerisomu monga mwa mabanja ao, motapa pa pfuko la Isakara, ndi pa pfuko la Aseri, ndi pa pfuko la Nafitali, ndi pa pfuko la Manase m'Basana, midzi khumi ndi itatu.
63 Ana a Merari analandira mwa maere monga mwa mabanja ao, motapa pa pfuko la Rubeni, ndi pa pfuko la Gadi, ndi pa pfuko la Zebuluni, midzi khumi ndi iwiri.
64 Ndipo ana a Israyeli anapatsa Alevi midzi ndi mabusa ao.
65 Ndipo anapatsa mwamaere, motapa pa pfuko la ana a Yuda, ndi pa pfuko la Simeoni, ndi pa pfuko la ana a Benjamini, midzi iyi yochulidwa maina ao.
66 Ndi mabanja ena a ana a Kohati anali nayo midzi ya malire ao, yotapa pa pfuko la Efraimu.