48 Ndipo kunali, pamene Mfilistiyo anadzikonza, nadza, nasendera pafupi kuti akomane ndi Davide, Davide anafulumira, nathamangira ku khamulo, kuti akomane ndi Mfilistiyo.
49 Ndipo Davide anapisa dzanja lace m'thumba mwace, naturutsamo mwala, nauponya, nalasa Mfilistiyo pamphumi; ndi mwalawo unalowa m'mphumi, ndipo iye anagwa pansi cafufumimba.
50 Comweco Davide anapambana Mfilistiyo ndi mwala wa coponyera cace, nakantha Mfilistiyo, namupha. Koma m'dzanja la Davide munalibe lupanga.
51 Potero Davide anathamanga naima pa Mfilistiyo, nagwira lupanga lace, nalisolola m'cimace, namtsiriza nadula nalo mutu wace. Ndipo pakuona Afilisti kuti ciwinda cao cidafa, anathawa.
52 Ndipo anthu a Israyeli ndi Ayuda ananyamuka, napfuula, nathamangira Afilistiwo, mpaka ufika kucigwako, ndi ku zipata za Ekroni. Ndipo Afilistiwo olasidwa anagwa pa njira ya ku Saraimu, kufikira ku Gad ndi ku Ekroni.
53 Ndipo ana a Israyeli atathamangira Afilisti, anabwerera nafunkha za m'zithando zao.
54 Ndipo Davide anatenga mutu wa Mfilistiyo, napita nao ku Yerusalemu; koma zida zace anazisunga m'hema wace.