4 Ndipo anyamata a Davide ananena naye, Onani, lero ndilo tsiku limene Yehova anati kwa inu, Onani, Ine ndidzapereka mdani wako m'dzanja lako, kuti ukamcitira iye cokukomera. Ndipo Davide ananyamuka, nadula mkawo wa mwinjiro wa Sauli mobisika.
5 Ndipo kunali m'tsogolo mwace kuti a mtima wa Davide unamtsutsa cifukwa adadula mkawo wa mwinjiro wa Sauli.
6 Nati kwa anyamata ace, Mulungu andiletse kucitira ici mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova, kumsamulira dzanja langa, popeza iye ndiye wodzozedwa wa Yehova.
7 Comweco Davide analetsa anyamata ace ndi mau awa, osawaloleza kuukira Sauli. Ndipo Sauli ananyamuka, naturuka m'phangamo, namuka njira yace.
8 Bwino lace Davide yemwe ananyamuka, naturuka m'phangamo, napfuulira Sauli, nati, Mbuye wanga, mfumu. Ndipo pakuceuka Sauli, Davide anaweramira nkhope yace pansi, namgwadira.
9 Davide nanena ndi Sauli, Bwanji mulikusamalira mau a anthu akuti, Onani, Davide afuna kukucitirani coipa.
10 Onani, lero lomwe maso anu anapenya kuti Yehova anakuperekani inu lero m'dzanja langa m'phangamo, ndipo ena anandiuza ndikupheni; koma ndinakulekani, ndi kuti, Sindidzatukulira mbuye wanga dzanja langa; cifukwa iye ndiye wodzozedwa wa Yehova.