2 Ndipo panali munthu ku Maoni, amene katundu wace anali ku Karimeli; iyeyu anali womveka ndithu, anali nazo nkhosa zikwi zitatu, ndi mbuzi cikwi cimodzi; ndipo analikusenga nkhosa zace ku Karimeli.
3 Tsono dzina la munthuyo ndiye Nabala, ndi dzina la mkazi wace ndiye Abigayeli; ndiye mkazi wa nzeru yabwino, ndi wa nkhope yokongola; koma mwamunayo anali waphunzo ndi woipa macitidwe ace; ndipo iye anali wa banja la Kalebi.
4 Ndipo Davide anamva kucipululu kuti Nabala alinkusenga nkhosa zace.
5 Davide natuma anyamata khumi, nanena kwa anyamatawo, Mukwere ku Karimeli, mumuke kwa Nabala ndi kundilankhulira iye;
6 ndipo muzitero kwa wodalayo, Mtendere ukhale pa inu, mtendere ukhalenso pa nyumba yanu, ndi mtendere ukhale pa zonse muli nazo.
7 Ndipo tsono ndamva kuti muli nao osenga nkhosa; abusa anu amene anali ndi ife, sitinawacititsa manyazi, ndipo panalibe kanthu kao kadasowa, nthawi yonse anakhala iwo ku Karimeli.
8 Mufunse anyamata anu, adzakuuzani; cifukwa cace muwakomere mtima anyamata awa, pakuti tirikufika tsiku labwino; mupatse ciri conse muli naco m'dzanja lanu, kwa anyamata anu, ndi kwa mwana wanu Davide.