1 Ndipo likasa la Yehova linakhala ku dziko la Afilisti miyezi isanu ndi iwiri.
2 Ndipo Afilistiwo anaitana ansembe ndi oombeza, nati, Ticitenji ndi likasa la Yehova? mutidziwitse cimene tilitumize naco kumalo kwace.
3 Ndipo iwo anati, Ngati mulitumiza kwina likasa la Mulungu wa Israyeli, musalitumize lopanda kanthu; koma makamaka mulibweze ndi nsembe yoparamula, mukatero mudzaciritsidwa, ndi kudziwa cifukwa cace dzanja lace liri pa inu losacoka.
4 Ndipo iwo aja anati, Tidzambwezera nsembe yoparamula yanji? Ndipo iwo anati, Mafundo asanu agolidi, ndi mbewa zisanu zagolidi, monga mwa ciwerengo ca mafumu a Afilisti; popeza kusauka kumodzi kunali pa inu nonse, ndi pa mafumu anu.
5 Cifukwa cace muzipanga zifanizo za mafundo anu, ndi zifanizo za mbewa zanu zimene ziipitsa dziko; ndipo mucitire ulemu Mulungu wa lsrayeli; kuti kapena adzaleza dzanja lace pa inu, ndi pa milungu yanu, ndi pa dziko lanu.
6 Mulikuumitsiranji mitima yanu, monga Aaigupto ndi Farao anaumitsa mitima yao? Kodi iwo sana lola anthuwo amuke, iye atacita kodabwitsa pakati pao, ndipo anamuka?