7 Ndipo pamene Afilisti anamva kuti Aisrayeli anasonkhana pamodzi ku Mizipa, mafumu a Afilisti anakwera kukayambana ndi Aisrayeli. Ndipo Aisrayeli pakumva ici, anacita mantha ndi Afilistiwo.
8 Ndipo ana a Israyeli anati kwa Samueli, Musaleke kutipempherera kwa Yehova Mulungu wathu, kuti iye atipulumutse m'manja a Afilistiwo.
9 Ndipo Samueli anatenga mwana wa nkhosa woyamwa, nampereka wathunthu kwa Yehova, nsembe yopsereza; ndipo Samueli anapempherera Israyeli kwa Yehova; ndipo Yehova anambvomereza.
10 Ndipo pamene Samueli analikupereka nsembe yopserezayo, Afilisti anayandikira kuti aponyane ndi Aisrayeli; koma tsiku lomwe lija Yehova anagunda ndi kugunda kwakukuru pa Afilistiwo, nawapolonganitsa. Ndipo anakanthidwa pamaso pa Aisrayeli.
11 Ndipo Aisrayeli anaturuka ku Mizipa, nathamangira Afilisti, nawakantha mpaka anafika pansi pa Betikara.
12 Pamenepo Samueli anatenga mwala nauimika pakati pa Mizipa ndi Seni, naucha dzina lace. Ebenezeri, nati, Kufikira pano Yehovaanatithandiza.
13 Comweco anagonjetsa Afilisti, ndino iwo sanatumphanso malire a Israyeli ndipo dzanja la Yehova linasautsa Afilisti masiku onse a Samueli.