4 Ndipo anapyola dziko lamapiri la Efraimu, napyola dziko la Salisa, koma sanawapeza; pamenepo anapyolanso dziko la Salimu; koma panalibe pamenepo, napyola dziko la Abenjamini, osawapeza.
5 Pamene anafika ku dziko la Zufi, Sauli anamuuza mnyamata amene anali naye, kuti, Tiye tibwerere; kuti atate wanga angaleke kusamalira aburuwo, ndi kutenga nkhawa cifukwa ca ife.
6 Koma ananena naye, Onatu, m'mudzi muno muli munthu wa Mulungu, ndiye munthu anthu amcitira ulemu; zonse azinena zicitika ndithu; tiyeni tipite komweko, kapena adzakhoza kutidziwitsa zimene tirikuyendera.
7 Ndipo Sauli ananena ndi mnyamata wace, Koma taona, tikapitako nmtengere ciani munthuyo? popeza mkate udatha m'zotengera zathu, ndiponso tiribe mphatso yakumtengera munthu wa Mulungu, tiri naco ciani?
8 Ndipo mnyamatayo anayankhanso kwa Sauli nati, Onani m'dzanja langa muli limodzi la magawo anai a sekeli wa siliva; ndidzampatsa munthu wa Mulungu limeneli kuti atiuze njira yathu.
9 Kale m'Israyeli, munthu akati afunse kwa Mulungu, adafotero kuti, Tiyeni tipite kwa mlauliyo; popeza iye wochedwa mneneri makono ano, anachedwa mlauli kale.
10 Pamenepo Sauli anati kwa mnyamata wace, Wanena bwino; tiye tipite. Comweco iwowa anapita kumudzi kumene kunali munthu wa Mulunguyo.