9 Tsopano, Yehova Mulungu, likhazikike lonjezano lanu la kwa Davide atate wanga; pakuti mwandiika mfumu ya anthu akucuruka ngati pfumbi lapansi.
10 Mundipatse tsono nzeru ndi cidziwitso, kuti ndituruke ndi kulowa pamaso pa anthu awa; pakuti angathe ndani kuweruza anthu anu awa ambiri?
11 Ndipo Mulungu anati kwa Solomo, Popeza cinali mumtima mwako ici, osapempha cuma, akatundu, kapena ulemu, kapena moyo wa iwo akudana nawe, osapemphanso masiku ambiri; koma wadzipemphera nzeru ndi cidziwitso, kuti uweruze anthu anga amene ndakuika ukhale mfumu yao,
12 nzeru ndi cidziwitso zipatsidwa kwa iwe, ndidzakupatsanso cuma, ndi akatundu, ndi ulemu, zotere zonga sanakhala nazo mafumu akale usanakhale iwe, ndi akudza pambuyo pako sadzakhala nazo zotero.
13 Momwemo Solomo anadza ku Yerusalemu kucokera ku msanje uli ku Gibeoni, ku khomo la cihema cokomanako; ndipo anacita ufumu pa Israyeli.
14 Ndipo Solomo anasonkhanitsa magareta ndi apakavalo, nakhala nao magareta cikwi cimodzi mphambu mazana anai, ndi apakavalo zikwi khumi ndi ziwiri; nawaika m'midzi ya magareta ndi kwa mfumu ku Yerusalemu.
15 Ndipo mfumu inatero kuti siliva ndi golidi zikhale m'Yerusalemu ngati miyala, ndi kuti mikungudza icuruke ngati mikuyu yokhala kucidikha.