11 nafukizira Yehova nsembe zopsereza m'mawa ndi m'mawa, ndi madzulo onse, ndi zonunkhira za pfungo lokoma, nakonza mkate woonekera pa gome lopatulika, ndi coikapo nyali cagolidi ndi nyali zace, ziyake madzulo onse; pakuti tisunga cilangizo ca Yehova Mulungu wathu, koma inu mwamsiya Iye.
12 Ndipo taonani, Mulungu ali nafe, wotitsogolera ndi ansembe ace, ndi malipenga oliza nao cokweza, kukulizirani inu cokweza. Ana a Israyeli inu, musalimbane naye Yehova Mulungu wa makolo anu; pakuti simudzapindula nako.
13 Koma Yerobiamu anazunguliritsa owalalira, awadzere kumbuyo; momwemo iwowa anali kumaso kwa Yuda, ndi owalalira anali kumbuyo kwao.
14 Ndipo poceuka Yuda, taonani, nkhondo inayambana nao kumaso ndi kumbuyo; napfuulira iwo kwa Yehova, ndi ansembe analiza malipenga.
15 Pamenepo amuna a Yuda anapfuula cokweza; ndipo popfuula amuna a Yuda, kunacitika kuti Mulungu anakantha Yerobiamu ndi Aisrayeli onse pamaso pa Abiya ndi Yuda.
16 Ndipo ana a Israyeli anathawa pamaso pa Yuda, nawapereka Mulungu m'dzanja lao.
17 Ndipo Abiya ndi anthu ace anawakantha makanthidwe akuru; nagwa, nafa amuna osankhika zikwi mazanaasanu a Israyeli.