1 Momwemo Abiya anagona ndi makolo ace, ndipo anamuika m'mudzi wa Davide; ndi Asa mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace, m'masiku ace dziko linaona bata zaka khumi.
2 Ndipo Asa anacita cokoma ndi coyenera m'maso mwa Yehova Mulungu wace,
3 nacotsa maguwa a nsembe acilendo, ndi misanje; naphwanya zoimiritsa zao, nalikha zifanizo zao,
4 nauza Yuda afune Yehova Mulungu wa makolo ao, ndi kucita cilamulo ndi cowauza, Iye.
5 Anacotsanso m'midzi yonse ya Yuda misanje, ndi zifanizo za dzuwa; ndi ufumuwo unacita bata pamaso pace.
6 Ndipo anamanga midzi yamalinga m'Yuda; pakuti dziko linacita bata, analibe nkhondo iyeyu zaka zija, popeza Yehova anampumulitsa.