10 Ndipo kuopsa kwa Yehova kunagwera maufumu a maiko ozungulira Yuda; momwemo sanayambana ndi Yehosafati.
11 Ndipo Afilisti ena anabweca nazo kwa Yehosafati mitulo, ndi ndalama za msonkho; Aarabu omwe anabwera nazo kwa iye zoweta, nkhosa zamphongo zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri ndi atonde zikwi zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi awiri.
12 Ndipo Yehosafati anakula cikulire, namanga m'Yuda nyumba zansanja, ndi midzi ya cuma.
13 Nakhala nazo nchito zambiri m'midzi ya Yuda, ndi anthu a nkhondo, ngwazi zamphamvu m'Yerusalemu.
14 Kuwerenga kwao monga mwa nyumba za atate ao ndiko: a Yuda, akuru a zikwi; Adina wamkuru, ndi pamodzi ndi iye ngwazi zamphamvu zikwi mazana atatu;
15 ndi wotsatana naye mkuru Yohanani, ndi pamodzi ndi iye zikwi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu;
16 ndi wotsatana naye Amasiya mwana wa Zikri, wodzipereka kwa Yehova mwaufulu, ndi pamodzi ndi iye ngwazi zamphamvu zikwi mazana awiri;