1 Yehosafati tsono anali nacocuma ndi ulemu zomcurukira, nacita cibale ndi Ahabu.
2 Ndipo zitatha zaka zina, anatsikira kwa Ahabu ku Samariya. Ndi Ahabu anamphera iye ndi anthu anali naye nkhosa, ndi ng'ombe zocuruka; namnyenga akwere naye pamodzi ku Ramoti Gileadi.
3 Nati Ahabu mfumu ya Israyeli kwa Yehosafati mfumu ya Yuda, Mupita nane kodi ku Ramoti Gileadi? Nayankha, nati, Monga inu momwemo ine; monga anthu anu momwemo anthu anga; tidzakhala nanu ku nkhondoyi.
4 Ndipo Yehosafati anati kwa mfumu ya Israyeli, Funsiranitu mau a Yehova lero lino.
5 Pamenepo mfumu ya Israyeli anamemeza aneneri amuna mazana anai, nanena nao, Kodi timuke kunkhondo ku Ramoti Gileadi kapena ndileke? Ndipo anati, Kweraniko, pakuti Mulungu adzaupereka m'dzanja la mfumu.
6 Koma Yehosafati anati, Kulibenso kuno mneneri wa Yehova, kuti tifunsire kwa iye?
7 Ndipo mfumu ya Israyeli inati kwa Yehosafati, Atsalanso munthu mmodzi, tifunsire Yehova kwa iye; koma ndimuda, pakuti sandinenera ine kanthu kokoma, koma zoipa nthawi zonse, ndiye Mikaya mwana wa Yimla. Nati Yehosafati, Isatero mfumu.