4 Ndipo Yehosafati anati kwa mfumu ya Israyeli, Funsiranitu mau a Yehova lero lino.
5 Pamenepo mfumu ya Israyeli anamemeza aneneri amuna mazana anai, nanena nao, Kodi timuke kunkhondo ku Ramoti Gileadi kapena ndileke? Ndipo anati, Kweraniko, pakuti Mulungu adzaupereka m'dzanja la mfumu.
6 Koma Yehosafati anati, Kulibenso kuno mneneri wa Yehova, kuti tifunsire kwa iye?
7 Ndipo mfumu ya Israyeli inati kwa Yehosafati, Atsalanso munthu mmodzi, tifunsire Yehova kwa iye; koma ndimuda, pakuti sandinenera ine kanthu kokoma, koma zoipa nthawi zonse, ndiye Mikaya mwana wa Yimla. Nati Yehosafati, Isatero mfumu.
8 Pamenepo mfumu ya Israyeli inaitana mdindo, niti, Katenge msanga Mikaya mwana wa Yimla.
9 Mfumu ya Israyeli tsono ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala yense pa mpando wacifumu wace, obvala zobvala zacifumu zao, nakhala pamalo poyera polowera pa cipata ca Samariya; ndi aneneri onse ananenera pamaso pao.
10 Ndipo Zedekiya mwana wa Kenana anadzisulira nyanga zacitsulo, nati, Atero Yehova, Ndi izi udzagunda Aaramu mpaka adatha psiti.