2 Pamenepo anadza anthu akuuza Yehosafati, kuti, Ukudzerani unyinji waukuru wa anthu ocokera tsidya la nyanja ku Aramu; ndipo taonani, ali ku Hazazoni Tamara, ndiwo Engedi.
3 Ndipo Yehosafati anacita mantha, nalunjikitsa nkhope yace kufuna Yehova, nalalikira kusala mwa Ayuda onse.
4 Namemezedwa Yuda afunsire kwa Yehova, inde anacokera ku midzi yonse ya Yuda kufuna Yehova.
5 Ndipo Yehosafati anaima mu msonkhano wa Ayuda, ndi a ku Yerusalemu, ku nyumba ya Yehova, pakati pa bwalo latsopano;
6 nati, Yehova Mulungu wa makolo athu, Inu sindinu Mulungu wa m'Mwamba kodi? sindinu woweruza maufumu onse a amitundu kodi? ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yolimba; palibe wina wakulaka Inu.
7 Sindinu Mulungu wathu, amene munainga nzika za m'dziko muno pa maso pa ana anu Israyeli, ndi kulininkha kwa mbeu ya Abrahamu bwenzi lanu kosatha?
8 nakhala m'mwemo iwowa, nakumangirani m'mwemo malo opatulika a dzina lanu, ndi kuti,