21 Ndipo atafunsana ndi anthu, anaika oyimbira Yehova, ndi kulemekeza ciyero cokometsetsa, pakuturuka iwo kutsogolera khamu la nkhondo, ndi kuti, Yamikani Yehova, pakuti cifundo cace cikhala cosatha.
22 Ndipo poyamba iwo kuyimba, ndi kulemekeza Yehova, anaika olalira alalire Aamoni, Amoabu, ndi a m'phiri la Seiri, akudzera Ayuda; ndipo anawakantha.
23 Pakuti ana a Amoni, ndi a Moabu, anaukira okhala m'phiri la Seiri, kuwapha ndi kuwaononga psiti; ndipo atatha okhala m'Seiri, anasandulikirana kuonongana.
24 Ndipo pofika Ayuda ku dindiro la kucipululu, anapenyera aunyinjiwo; taonani, mitembo iri ngundangunda, wosapulumuka ndi mmodzi yense.
25 Ndipo pofika Yehosafati ndi anthu ace kutenga zofunkha zao, anapezako cuma cambiri, ndi mitembo yambiri, ndi zipangizo zofunika, nadzifunkhira, osakhoza kuzisenza zonse; nalimkutenga zofunkhazo masiku atatu, popeza zinacuruka.
26 Ndi tsiku lacinai anasonkhana m'cigwa ca Beraka; pakuti pamenepo analemekeza Yehova; cifukwa cace anacha dzina lace la malowo, Cigwa ca Beraka, mpaka lero lino.
27 Pamenepo anabwerera amuna onse a Yuda, ndi a ku Yerusalemu, nawatsogolera ndi Yehosafati, kubwerera kumka ku Yerusalemu ndi cimwemwe; pakuti Yehova anawakondweretsa pa adani ao.