1 Ndipo okhala m'Yerusalemu anamlonga Ahaziya mwana wace wamng'ono akhale mfumu m'malo mwace; pakuti gulu la anthu, adadzawo pamodzi ndi Aarabu kucigono, adapha ana oyamba onse. Momwemo Ahaziya mwana wa Yehosafati anakhala mfumu ya Yuda.
2 Ahaziya anali wa zaka makumi anai mphambu ziwiri polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu caka cimodzi; ndi dzina la mace ndiye Ataliya mwana wa Omri.
3 Iyenso anayenda m'njira za nyumba ya Ahabu; pakuti wompangira ndi mace acite coipa,
4 Ndipo anacita coipa pamaso pa Yehova, monga umo anacitira a nyumba ya Ahabu; pakuti ompangira ndi iwowa, atamwalira atate wace; ndi kuonongeka kwace nkumeneko.
5 Anayendanso m'kupangira kwao, namuka pamodzi ndi Yehoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israyeli, kukayambana nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya Aramu ku Ramoti Gileadi; ndipo Aaramu anamlasa Yehoramu.