11 Pamenepo anaturutsa mwana wa mfumu, nambveka korona, nampatsa mboni, namlonga ufumu; ndi Yehoyada ndi ana ace anamdzoza, nati, Ikhale ndi moyo mfumu.
12 Ndipo pamene Ataliya anamva phokoso la anthu alikuthamanga ndi kulemekeza mfumu, anadza kwa anthu m'nyumba ya Yehova;
13 napenya, ndi kuona mfumu inaima pa nsanamira yace polowera; ndi atsogoleri, ndi malipenga, anali kwa mfumu; ndi anthu onse a m'dziko anakondwera, naomba amalipenga; oyimbira omwe analiko ndi zoyimbirazo, nalangiza poyimbira colemekeza. Pamenepo Ataliya anang'amba zobvala zace, nati, Ciwembu, ciwembu.
14 Koma Yehoyada wansembe anaturuka nao atsogoleri a mazana akuyang'anira khamu la nkhondo, nanena nao, Mturutseni mkaziyo pakati pa mipambo; ndipo ali yense womtsata aphedwe ndi lupanga; pakuti wansembe adati, Msamphere m'nyumba ya Yehova.
15 Ndipo anampisa malo; namuka iye kolowera ku cipata ca akavalo kunyumba ya mfumu; ndi pomwepo anamupha.
16 Ndipo Yehoyada anacita pangano pakati pa iye, ndi anthu onse, ndi mfumu, kuti adzakhala anthu a Yehova.
17 Ndi anthu onse anamuka ku nyumba ya Baala, naipasula, naphwanya maguwa ace a nsembe, ndi mafano ace; namupha Matana wansembe wa Baala ku maguwa a nsembe.