16 Ndipo Yehoyada anacita pangano pakati pa iye, ndi anthu onse, ndi mfumu, kuti adzakhala anthu a Yehova.
17 Ndi anthu onse anamuka ku nyumba ya Baala, naipasula, naphwanya maguwa ace a nsembe, ndi mafano ace; namupha Matana wansembe wa Baala ku maguwa a nsembe.
18 Ndipo Yehoyada anaika mayang'aniro a nyumba ya Yehova m'dzanja la ansembe Aleviwo, amene Davide anawagawa, ayang'anire nyumba ya Yehova; napereka nsembe zopsereza za Yehova monga mulembedwa m'cilamulo ca Mose, ndi kukondwera ndi kuyimbira, monga mwa cilangizo ca Davide.
19 Ndipo anaika odikira ku makomo a nyumba ya Yehova, kuti wodetsedwa nako kanthu kali konse asalowemo.
20 Natenga atsogoleri a mazana, ndi omveka, ndi akazembe a anthu, ndi anthu onse a m'dziko, natsika ndi mfumu ku nyumba ya Yehova; nalowera pa cipata ca kumtunda m'nyumba ya mfumu, namkhalitsa mfumu pa mpando wa ufumu.
21 Ndipo anthu onse a m'dziko anakondwera; ndi m'mudzi munali cete, atamupha Ataliya ndi lupanga.