6 Koma asalowe mmodzi m'nyumba ya Yehova, ansembe okha, ndi Alevi otumikira, alowe iwowa; pakuti ndiwo opatulika; koma anthu onse asunge udikiro wa Yehova.
7 Ndipo Alevi amzinge mfumu pozungulirapo, yense ndi zida zace m'dzanja mwace; ndipo ali yense wolowa m'nyumba aphedwe; nimukhale inu pamodzi ndi mfumu pakulowa ndi pakuturuka iye.
8 Momwemo Alevi ndi Ayuda onse anacita monga mwa zonse anawauza Yehoyada wansembe; natenga yense amuna ace alowe dzuwa la Sabata pamodzi ndi oturuka dzuwa la Sabata; pakuti Yehoyada wansembe sanamasula zigawo.
9 Ndi Yehoyada wansembe anapereka kwa akazembe a mazana mikondo, ndi zikopa, ndi maraya acitsulo, zinali za mfumu Davide, zokhala m'nyumba, ya Mulungu.
10 Ndipo anaika anthu onse, yense ndi cida cace m'dzanja lace, amzinge mfumu, kuyambira mbali ya ku dzanja lamanja la nyumba kufikira mbali ya ku dzanja lamanzere la nyumba, kuloza ku guwa la nsembe ndi kunyumba.
11 Pamenepo anaturutsa mwana wa mfumu, nambveka korona, nampatsa mboni, namlonga ufumu; ndi Yehoyada ndi ana ace anamdzoza, nati, Ikhale ndi moyo mfumu.
12 Ndipo pamene Ataliya anamva phokoso la anthu alikuthamanga ndi kulemekeza mfumu, anadza kwa anthu m'nyumba ya Yehova;