19 Koma Iye anawatumira aneneri kuwabwezeranso kwa Yehova, ndiwo anawacitira umboni; koma sanawamvera.
20 Ndipo mzimu wa Mulungu unabvala Zekariya mwana wa Yehoyada wansembe, naima iye kumtunda kwa anthu, nanena nao, Atero Mulungu, Mulakwiranji malamulo a Yehova kuli kosalemerera nako? Popeza mwasiya Yehova, Iye wasiyanso inu.
21 Koma anampangira ciwembu, namponya miyala, mwa lamulo la mfumu m'bwalo la nyumba ya Yehova.
22 Motero mfumu Yoasi sanakumbukila zokoma anamcitirazi Yehoyada atate wace, koma anapha mwana wace; ndiye pomwalira anati, Yehova acipenye, nacifunse.
23 Ndipo kunacitika, podzanso nyengoyi khamu la nkhondo la Aaramu linamkwerera, nafika iwo ku Yuda ndi Yerusalemu, naononga mwa anthu akalonga onse a anthu, natumiza zofunkha zao zonse kwa mfumu ya ku Damasiko.
24 Pakuti khamu la nkhondo la Aaramu linadza la anthu owerengeka; ndipo Yehova anapereka khamu lalikuru m'dzanja lao; popeza adasiya Yehova Mulungu wa makolo ao. Motero anacitira Yoasi zomlanga.
25 Ndipo atamcokera (popeza anamsiya wodwala nthenda zazikuru), anyamata ace anamcitira ciwembu, cifukwa ca mwazi wa ana a Yehoyada wansembe, namupha pakama pace, namwalira iye; ndipo anamuika m'mudzi wa Davide, koma osamuika m'manda a mafumu.