4 Ndipo pambuyo pace mumtima mwa Yoasi munali cofuna kukonzanso nyumba ya Yehova.
5 Nasonkhanitsa ansembe ndi Alevi, nanena nao, Muturuke kumka ku midzi ya Yuda, ndi kusonkhanitsa kwa Aisrayeli onse ndarama zakukonzetsa nyumba ya Mulungu wanu caka ndi caka; ndipo inu fulumirani nayo nchitoyi. Koma Alevi sanafulumira nayo.
6 Ndipo mfumu inaitana Yehoyada mkuru wao, niti naye, Unalekeranji kuuza Alevi abwere nao kucokera m'Yuda ndi Yerusalemu msonkho wa Mose mtumiki wa Yehova, ndi wa msonkhano wa Israyeli, ukhale wa cihema ca umboni?
7 Pakuti ana a Ataliya mkazi woipa uja anathyola citseko ca nyumba ya Mulungu, natenga zopatulidwa zonse za nyumba ya Yehova kuzipereka kwa Baala.
8 Nilamulira mfumu, ndipo anapanga bokosi, naliika kunja ku cipata ca nyumba ya Yehova.
9 Nalalikira mwa Yuda ndi Yerusalemu, abwere nao kwa Yehova msonkho umene Mose mtumiki wa Mulungu anauikira Aisrayeli m'cipululu.
10 Ndipo akalonga onse ndi anthu onse anakondwera, nabwera nazo, naponya m'bokosi mpaka atatha.