14 Pamenepo eni zida anasiya andende ndi zofunkha pamaso pa akalonga ndi msonkhano wonse.
15 Nanyamuka amuna ochulidwa maina, natenga andende, nabveka ausiwa onse mwa iwo ndi zofunkhazo, nawapatsa zobvala, ndi nsapato, nawadyetsa ndi kuwamwetsa, nawadzoza, nasenza ofoka ao onse pa aburu, nafika nao ku Yeriko, mudzi wa migwalangwa, kwa abale ao; nabwerera iwo kunka ku Samariya.
16 Nthawi yomweyi mfumu Ahazi anatumiza kwa mafumu a Asuri amthandize.
17 Pakuti Aedomu anadzanso, nakantha Yuda, natenga andende.
18 Afilisti omwe adagwa m'midzi ya kucidikha, ndi ya kumwela kwa Yuda, nalanda Betisemesi, ndi Azaloni, ndi Gederoti, ndi Soko ndi miraga yace, ndi Timna ndi miraga yace; nakhala iwo komweko.
19 Pakuti Yehova anacepetsa Yuda cifukwa ca Ahazi mfumu ya Israyeli; popeza iye anacita comasuka pakati pa Yuda, nalakwira Yehova kwambiri.
20 Ndipo Tigilati Pilesere mfumu ya Asuri anadza kwa iye, namsautsa osamlimbikitsa.