1 Citatha ici conse tsono, Aisrayeli onse opezekako anaturuka kumka ku midzi ya Yuda, naphwanya zoimiritsa, nalikha zifanizo, nagamula misanje ndi maguwa a nsembe m'Yuda monse, ndi m'Benjamini, m'Efraimunso, ndi m'Manase, mpaka adaziononga zonse. Pamenepo ana onse a Israyeli anabwerera, yense ku dziko lace ndi ku midzi yao.
2 Ndipo Hezekiya anaika zigawo za ansembe ndi Alevi, monga mwa magawidwe ao, yense monga mwa utumiki wace, ndi ansembe ndi Alevi, acite nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika kutumikira, ndi kuyamika, ndi kulemekeza, ku zipata za cigono ca Ambuye.
3 Naikanso gawo la mfumu lotapa pa cuma cace la nsembe zopsereza, ndilo la nsembe zopsereza za m'mawa ndi madzulo, ndi la nsembe zopsereza za masabata, ndi za pokhala mwezi, ndi za nyengo zoikika, monga mulembedwa m'cilamulo ca Yehova.
4 Anauzanso anthu okhala m'Yerusalemu apereke gawo la ansembe ndi Alevi, kuti iwowa alimbike m'cilamulo ca Yehova.