8 Ndipo pamene Hezekiya ndi akuru ace anadza, naona miyuruyi, analemekeza Yehova, nadalitsa anthu ace Aisrayeli.
9 Pamenepo Hezekiya anafunsana ndi ansembe ndi Alevi za miyuruyi,
10 Ndipo Azariya wansembe wamkuru wa nyumba ya Zadoki anamyankha, nati, Ciyambire anthu anabwera nazo zopereka ku nyumba ya Yehova, tadya, takhuta, ndipo zatitsalira zambiri; pakuti Yehova anadalitsa anthu ace; ndipo suku kucuruka kwa cotsala.
11 Pamenepo Hezekiya anawauza akonze zipinda m'nyumba ya Yehova; nazikonza.
12 Ndipo anabwera nazo nsembe zokweza, ndi amodzi a magawo khumi, ndi zinthu zopatulika, mokhulupirika; ndi mkuru woyang'anira izi ndiye Konaniya Mlevi, ndi Simei mng'ono wace ndiye wotsatana naye.
13 Ndi Yeiyeli, ndi Azaziya, ndi Nahati, ndi Asaheli, ndi Yerimoti, ndi Yozabadi, ndi Eliyeli, ndi Ismakiya, ndi Mahati, ndi Benaya, ndiwo akapitao omvera Konaniya ndi Simei mng'ono wace, oikidwa ndi Hezekiya mfumu ndi Azariya mkuru wa ku nyumba ya Mulungu.
14 Ndipo Kore mwana wa Imna Mlevi, wa ku cipata ca kum'mawa, anayang'anira zopereka zaufulu za Mulungu, kugawira nsembe zokweza za Yehova, ndi zopatulikitsa.