1 Zitatha zinthu izi zokhulupirika, anadza Sanakeribu mfumu ya Asuri, nalowera Yuda, namangira midzi yamalinga misasa, nati adzigonjetsere iyi.
2 Ndipo pakuona Hezekiya kuti wadza Sanakeribu, ndi kuti nkhope yace inalunjikitsa kuyambana nkhondo ndi Yerusalemu,
3 anapangana ndi akuru ace ndi amphamvu ace, kutseka madzi a m'akasupe okhala kunja kwa mudzi; namthandiza iwo.
4 Nasonkhana anthu ambiri, natseka akasupe onse, ndi mtsinje woyenda pakati pa dziko, ndi kuti, Angafike mafumu a Asuri ndi kupeza madzi ambiri.
5 Ndipo analimbika mtima, namangitsa linga lonse mopasuka, nalikweza mpaka pansanja, ndi linga lina kunja kwace, nalimbitsa Milo m'mudzi wa Davide, napanga zida ndi zikopa zocuruka.
6 Naika akazembe a nkhondo alamulire anthu, nawasonkhanitsira kuli iye ku bwalo la ku cipata ca mudzi, nanena nao motonthoza mtima wao ndi kuti,
7 Limbani, mulimbike mtima, musaopa kapena ku tenga nkhawa pankhope pa mfumu ya Asuri ndi aunyinji okhala naye; pakuti okhala nafe acuruka koposa okhala naye;