1 Manase anali wa zaka khumi ndi ziwiri polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi asanu mphambu zisanu.
2 Nacita coipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonyansa za amitundu, amene Yehova anawacotsa m'dziko mwao pamaso pa ana a Israyeli.
3 Pakuti anamanganso misanje adaipasula Hezekiya atate wace, nautsira Abaala maguwa a nsembe, napanga zifanizo, nalambira khamu lonse la kuthambo, nalitumikira.
4 Namanga maguwa a nsembe m'nyumba ya Yehova, imene Yehova adati, M'Yerusalemu mudzakhala dzina langa ku nthawi zonse.
5 Namangiranso khamu lonse la kuthambo maguwa a nsembe m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehoya.