14 Ndiponso ansembe akulu onse ndi anthu anacurukitsa zolakwa zao, monga mwa zonyansa zonse za amitundu, nadetsa nyumba ya Yehova, imene ana patula m'Yerusalemu.
15 Ndipo Yehova Mulungu wa makolo ao anatumiza kwa iwo, ndi dzanja la mithenga yace, nalawirira mamawa kuituma, cifukwa anamvera cifundo anthu ace, ndi pokhala pace;
16 koma ananyodola mithenga ya Mulungu, napeputsa mau ace, naseka aneneri ace, mpaka ukali wa Mulungu unaukira anthu ace, mpaka panalibe colanditsa.
17 Pakuti Iye anawakweretsera mfumu ya Akasidi, ndiye anawaphera anyamata ao ndi lupanga, m'nyumba ya malo ao opatulika, osacitira cifundo mnyamata kapena namwali, mkulu kapena nkhalamba; Mulungu anawapereka onse m'dzanja lace.
18 Ndi zipangizo zonse za nyumba ya Mulungu, zazikuru ndi zazing'ono, ndi cuma ca nyumba ya Yehova, ndi cuma ca mfumu, ndi ca akalonga ace, anabwera nazo zonsezi ku Babulo.
19 Ndipo anatentha nyumba ya Mulungu, nagumula linga la Yerusalemu, natentha nyumba zace zonse zacifumu ndi moto, naononga zipangizo zace zonse zokoma.
20 Ndi iwo amene adapulumuka kulupanga anamuka nao ku Babulo, nakhala iwo anyamata ace, ndi a ana ace, mpaka mfumu ya Perisiya idacita ufumu;