2 Yehoahazi anali wa zaka makumi awiri mphambu zitatu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu miyezi itatu.
3 Ndipo mfumu ya Aigupto anamcotsera ufumu wace m'Yerusalemu, nasonkhetsa dziko matalente zana limodzi a siliva, ndi talente limodzi la golidi.
4 Ndi mfumu ya Aigupto anamlonga Eliyakimu mng'ono wace mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu, nasintha dzina lace likhale Yehoyakimu. Koma Neko anatenga Yehoahazi mkuru wace, namuka naye ku Aigupto.
5 Yehoyakimu anali wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka khumi ndi cimodzi, nacita coipa pamaso pa Yehova Mulungu wace.
6 Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo anakwera kuyambana naye, nammanga ndi matangadza kumuka naye ku Babulo.
7 Nebukadinezara anatenganso zipangizo za nyumba ya Yehova kumka nazo ku Babulo, naziika m'kacisi wace ku Babulo.
8 Macitidwe ena tsono a Yehoyakimu, ndi zonyansa zace anazicita, ndi zija zidapezeka zomtsutsa; taonani, zilembedwa m'buku la mafumu a Israyeli ndi Yuda; ndi Yehoyakini mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.