1 PANALI munthu m'dziko la Uzi, dzina lace ndiye Yobu; ndipo munthuyu anali wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.
2 Ndipo anabala ana amuna asanu ndi awiri, ndi ana akazi atatu.
3 Zoweta zacenso zinali nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi ngamila zikwi zitatu, ndi ng'ombe zamagoli mazana asanu, ndi aburu akazi mazana asanu, anchito ace omwe ndi ambiri; cotero munthuyu anaposa anthu onse'a kum'mawa.
4 Ndipo ana ace amuna anamuka kukacita madyerero m'nyumba ya yense pa tsiku lace; natumiza mthenga kuitana alongo ao atatu adzadye nadzamwe nao.
5 Ndipo kunatero, atatha masiku a madyererowa Yobu anatumiza mau, nawapatula, nauka mamawa, nafukiza nsembe zopsereza, monga mwa kuwerenga kwa iwo onse; pakuti Yobu anati, Kapena anacimwa ana anga, nacitira Mulungu mwano m'mtima mwao. Anatero Yobu masiku onse.
6 Ndipo panali tsiku lakuti ana a Mulungu anadza kudzionetsa kwa Yehova, nadzanso Satana pakati pao.
7 Nati Yehova kwa Satana, Ufuma kuti? Nayankha Satana kwa Yehova, nati, Kupitapita m'dziko ndi kuyendayenda m'mwemo.