18 ndipo anaitana nafunsa ngati Simoni, wochedwanso Petro, acerezedwako.
19 Ndipo m'mene Petro analingirira za masomphenya, Mzimu ananena naye, Taona, amuna atatu akufuna iwe.
20 Komatu tauka, nutsike, ndipo upite nao, wosakayika-kayika; pakuti ndawatuma ndine.
21 Ndipo Petro anatsikira kwa anthuwo, nati, Taonani, ine ndine amene mumfuna; cifukwa cace mwadzera nciani?
22 Ndipo anati, Komeliyo kenturiyoyo, munthu wolungama ndi wakuopa Mulungu, amene mtundu wonse wa Ayuda umcitira umboni, anacenjezedwa ndi mngelo woyera kuti atumize nakuitaneni mumuke ku nyumba yace, ndi kummvetsa mau anu.
23 Pamenepo anawalowetsa nawacereza.Ndipo m'mawa mwace ananyamuka naturuka nao, ndi ena a abale a ku Yopaanamperekezaiye.
24 Ndipo m'mawa mwace analowa m'Kaisareya, Koma Komeliyo analikudikira iwo, atasonkhanitsa abale ace ndi mabwenzi ace eni eni.