33 Ndipo anawatenga ora lomwelo la usiku, natsuka mikwingwirima yao; nabatizidwa pomwepo, iye ndi a pabanja pace.
34 Ndipo anakwera nao kunka kunyumba kwace, nawakhazikira cakudya, nasangalala kwambiri, pamodzi ndi a pabanja pace, atakhulupirira Mulungu.
35 Kutaca, oweruza anatumiza akapitao, kuti, Mukamasule anthu aja.
36 Ndipo mdindo anafotokozera mauwo kwa Paulo, nati, Oweruza atumiza mau kunena kuti mumuke; tsopanotu turukani, mukani mumtendere.
37 Koma Paulo anati kwa iwo, Adatikwapula ire pamaso pa anthu, osamva mlandu wathu, ire amene tiri Aroma, natiika m'ndende; ndipo tsopano kodi afuna kutiturutsira ire m'tseri? Iai, ndithu; koma adze okha atiturutse.
38 Ndipo akapitao anafotokozera mauwo kwa oweruza; ndipo iwowo anaopa, pakumva kuti anali Aroma.
39 Ndipo anadza nawapembedza; ndipo pamene anawaturutsa, anawapempha kuti acoke pamudzi.