3 ndipo popeza anali wa nchito imodzimodzi, anakhala nao, ndipo iwowa anagwira nchito; pakuti nchito yao inali yakusoka mahema.
4 Ndipo anafotokozera m'sunagogemasabata onse, nakopa Ayuda ndi Ahelene.
5 Koma pamene Sila ndi Timoteo anadza potsika ku Makedoniya, Paulo anapsinjidwa ndi mau, nacitira umboni kwa Ayuda kuti Yesu ndiye Kristu.
6 Koma pamene iwo anamkana, nacita mwano, anakutumula maraya ace, nati kwa iwo, Mwazi wanu ukhale pa mitu yanu; ine ndiribe kanthu; kuyambira tsopano ndinka kwa amitundu.
7 Ndipo anacoka kumeneko, nalowa m'nyumba ya munthu, dzina lace Tito Yusto, amene anapembedza Mulungu, nyumba yace inayandikizana ndi sunagoge.
8 Ndipo Krispo, mkuru wasunagoge, anakhulupirira Ambuye, ndi apabanja ace onse; ndipo Akorinto ambiri anamva, nakhulupira, nabatizidwa.
9 Ndipo Ambuye anati kwa Paulo usiku m'masomphenya, Usaope, koma nena, usakhale cete;