1 Ndipo kunali, titalekana nao ndi kukankha ngalawa, tinadza molunjika ku Ko, ndi m'mawa mwace ku Rode, ndipo pocokerapo ku Patara;
2 ndipo m'mene tinapeza ngalawa Yakuoloka kunka ku Foinike, tinalowamo, ndi kupita nayo.
3 Ndipo pamene tinafika popenyana ndi Kupro, tinacisiya kulamanzere, ntinapita ku Suriya; ndipo tinakoceza ku Turo; pakuti pamenepo ngalawainafuna kutula akatundu ace.
4 Ndipo m'mene tinapeza ophunzira, tinakhalako masikuasanu ndi awiri; ndipo iwowa ananena ndi Paulo mwa Mzimu, kuti asakwere ku Yerusalemu.