4 Ndipo m'mene tinapeza ophunzira, tinakhalako masikuasanu ndi awiri; ndipo iwowa ananena ndi Paulo mwa Mzimu, kuti asakwere ku Yerusalemu.
5 Ndipo kunali pamene tidatsiriza masikuwa, tidacoka ndi kunka ulendo wathu; ndipo iwo onse, akazi ndi ana anatiperekeza kufikira kuturuka m'mudzi; ndipo pogwadira pa mcenga wa kunyanja, tinapemphera,
6 ndi kulawirana; ndipo tinalowa m'ngalawa, koma iwo anabwera kwao.
7 Ndipo ife titatsiriza ulendo wathu wocokera ku Turo, tinafika ku Ptolemayi; ndipo m'mene tidalankhula abale, tinakhala nao tsiku limodzi.
8 Ndipo m'mawa mwace tinacoka, ntinafika ku Kaisareya, ndipo m'mene tinalowa m'nyumba ya Filipo mlaliki, mmodzi wa asanu ndi awiri aja, tinakhala naye.
9 Ndipo munthuyu anali nao ana akazi anai, anamwali, amene ananenera.
10 Ndipo pokhalapo masiku ambiri, anatsika ku Yudeya mneneri, dzina lace Agabo.