10 namlanditsa iye m'zisautso zace zonse, nampatsa cisomo ndi nzeru pamaso pa Farao mfumu ya ku Aigupto; ndipo anamuika iye kazembe wa pa Aigupto ndi pa nyumba yace yonse.
11 Koma inadza njala pa Aigupto ndi Kanani lonse, ndi cisautso cacikuru; ndipo sanapeza cakudya makolo athu.
12 Koma pakumva Yakobo kuti muli tirigu m'Aigupto, anatuma makolo athu ulendo woyamba,
13 Ndipo pa ulendo waciwiri Y osefe anazindikirika ndi abale ace; ndipo pfuko la Yosefe linaonekera kwa Farao.
14 Ndipo Yosefe anatumiza, naitana Yakobo atate wace, ndi a banja lace lonse, ndiwo anthu makumi asanu ndi awiri mphambu asanu.
15 Ndipo Yakobo anatsikira ku Aigupto; ndipo anamwalira, iye ndi makolo athu;
16 ndipo anawanyamula kupita nao ku Sukemu, nawaika m'manda amene Abrahamu adagula ndi mtengo wace wa ndalama kwa ana a Emori m'Sukemu.