5 ndipo sanampatsa colowa cace m'menemo, ngakhale popondapo phazi lace iai; ndipo anamlonjezera iye kuti adzampatsa ili, likhale lace, ndi la mbeu yace yomtsatira, angakhale analibe mwana pamenepo.
6 Koma Mulungu analankhula cotero, kuti mbeu yace idzakhala alendo m'dziko la eni, ndipo adzawacititsa ukapolo, nadzawacitira coipa, zaka mazana anai.
7 Ndipo mtundu amene udzawayesa akapolo, ndidzauweruza Ine, anatero Mulungu; ndipo zitapita izi adzaturuka, nadzanditumikira Ine m'malo muno.
8 Ndipo anaiupatsa iye cipangano ca mdulidwe; ndipo kotero Abrahamu anabala Isake, namdula tsiku lacisanu ndi citatu; ndi Isake anabala Yakobo, ndi Yakobo anabala makolo akulu aja khumi ndi awiri.
9 Ndipo makolo akuluwa podukidwa naye Yosefe, anamgulitsa amuke naye ku Aigupto; ndipo Mulungu anali naye,
10 namlanditsa iye m'zisautso zace zonse, nampatsa cisomo ndi nzeru pamaso pa Farao mfumu ya ku Aigupto; ndipo anamuika iye kazembe wa pa Aigupto ndi pa nyumba yace yonse.
11 Koma inadza njala pa Aigupto ndi Kanani lonse, ndi cisautso cacikuru; ndipo sanapeza cakudya makolo athu.