1 Ndipo zitatha izi, Nahasi mfumu ya ana a Amoni anamwalira, ndi mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.
2 Ndipo Davide anati, Ndidzamcitira zokoma mtima Hanuni mwana wa Nahasi, popeza atate wace anandicitira ine zokoma mtima. Momwemo Davide anatuma mithenga imtonthoze mtima pa atate wace. Pofika anyamata ace a Davide ku dziko la ana a Amoni kwa Hanuni kumtonthoza mtima,
3 akalonga a ana a Amoni anati kwa Hanuni, Davide ali kucitira atate wanu ulemu kodi, popeza anakutumizirani otonthoza? sakudzerani kodi anyamata ace kufunafuna, ndi kugubuduza, ndi kuzonda dziko?
4 Ndipo Hanuni anatenga anyamata a Davide, nawameta, nadula malaya ao pakati kufikira m'matako, nawaleka acoke.
5 Pamenepo anamuka ena, namuuza Davide za amunawa. Natumiza iye kukomana nao, pakuti amunawa anacita manyazi kwambiri. Ndipo mfumu inati, Balindani ku Yeriko mpaka zamera ndebvu zanu; zitamera mubwere.
6 Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, Hanuni ndi ana a Amoni anatumiza matalente cikwi cimodzi a siliva, kudzilembera magareta ndi apakavalo ku Mesopotamiya, ndi ku Aramu-maaka, ndi ku Zoba.
7 Momwemo anadzilembera magareta zikwi makumi atatu mphambu ziwiri, ndi mfumu ya Maaka ndi anthu ace; nadza iwo, namanga misasa cakuno ca Medeba. Ana a Amoni omwe anasonkhana m'midzi mwao, nadza kunkhondo.