6 Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti anadzinunkhitsa kwa Davide, Hanuni ndi ana a Amoni anatumiza matalente cikwi cimodzi a siliva, kudzilembera magareta ndi apakavalo ku Mesopotamiya, ndi ku Aramu-maaka, ndi ku Zoba.
7 Momwemo anadzilembera magareta zikwi makumi atatu mphambu ziwiri, ndi mfumu ya Maaka ndi anthu ace; nadza iwo, namanga misasa cakuno ca Medeba. Ana a Amoni omwe anasonkhana m'midzi mwao, nadza kunkhondo.
8 Pamene Davide anamva ici anatuma Yoabu ndi gulu lonse la anthu amphamvu.
9 Ndipo ana a Amoni anaturuka, nandandalitsa nkhondo ku cipata ca mudzi, ndi mafumu adadzawo anali pa okha kuthengo.
10 Pakuona Yoabu tsono kuti nkhondo inamdzera kumaso ndi kumbuyo, anasankha amuna osankhika onse a Israyeli, nawanika ayambane ndi Aaramu.
11 Ndipo anthu otsala anawapereka m'dzanja la Abisai mbale wace; ndipo anadzinika avambane ndi ana a Amoni.
12 Ndipo anati, Akandilaka Aaramu, udzandilanditsa ndiwe; koma akakulaka ana a Amoni, ndidzakulanditsa ndine.