19 Ndipo Davide anakwera monga mwa mau a Gadi adawanena m'dzina la Yehova.
20 Poceuka Orinani anaona wamthengayo; ndi ana ace amuna anai anali naye anabisala. Koma Orinani analikupuntha tirigu.
21 Ndipo pofika Davide kwa Orinani, Orinaniyo anapenyetsa, naona Davide, naturuka kudwale, nawerama kwa Davide, nkhope yace pansi.
22 Davide tsono anati kwa Orinani, Ndipatse padwale pano kuti ndimangepo guwa la nsembe la Yehova; undipatse gi pa mtengo wace wonse, kuti mliri ulekeke pa anthu.
23 Ndipo Orinani anati kwa Davide, Mulitenge, ndi mbuye wanga mfumu icite comkomera m'maso mwace; taonani, ndikupatsani ng'ombe za nsembe zopsereza; ndi zipangizo zopunthira zikhale nkhuni, ndi tirigu wa nsembe yaufa; ndizipereka zonse.
24 Koma mfumu Davide anati kwa Orinani, lai, koma ndidzaligula pa mtengo wace wonse; pakuti sindidzatengera Yehova ciri cako, kapena kupereka nsembe yopsereza yopanda mtengo wace.
25 Momwemo Davide anapatsa Orinani cogulira malowa golidi wa masekeli mazana asanu ndi limodzi kulemera kwace.