17 Ndidziwanso, Mulungu wanga, kuti muyesa mtima, nimukondwera nako kuongoka. Kama ine, ndi mtima wanga woongoka ndapereka zonsezi mwaufulu; ndipo tsopano ndaona mokondwera anthu anu okhala pompano, napereka kwa Inu mwaufulu.
18 Yehova Mulungu wa Abrahamu, wa Isake, ndi wa Israyeli makolo athu, musungitse ici kosatha m'cilingaliro ca maganizo a mtima wa anthu anu, nimulunjikitse mitima yao kwanu,
19 nimupatse Solomo mwana wanga mtima wangwiro kusunga malamulo anu, mboni zanu, ndi malemba anu, ndi kucita izi zonse, ndi kumanga cinyumbaci cimene ndakonzeratu mirimo yace,
20 Ndipo Davide anati kwa khamu lonse, Mulemekeze tsono Yehova Mulungu wanu. Ndi khamu lonse linalemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao, nawerama, nalambira Yehova, ndi mfumu.
21 Ndipo anamphera Yehova nsembe, napereka nsembe zopsereza kwa Yehova m'mawa mwace mwa tsiku lija, ndizo ng'ombe cikwi cimodzi, nkhosa zamphongo cikwi cimodzi, ndi ana a nkhosa cikwi cimodzi, pamodzi ndi nsembe zao zothira, ndi nsembe zocuruka za Aisrayeli onse:
22 nadya namwa pamaso pa Mulungu tsiku lomwelo ndi cimwemwe cacikuru. Ndipo analonga ufumu Solomo mwana wa Davide kaciwiri, namdzozera Yehova akhale kalonga, ndi Zadoki akhale wansembe.
23 Momwemo Solomo anakhala pa mpando wacifumu wa Yehova, ndiye mfumu m'malo mwa Davide atate wace, nalemerera, nammvera iye Aisrayeli onse.