3 Ndiponso popeza ndikondwera nayo nyumba ya Mulungu wanga, cuma cangacanga ca golidi ndi siliva ndiri naco ndicipereka ku nyumba ya Mulungu wanga, moenjezera ndi zonse ndazikonzeratu nyumba yopatulikayo;
4 ndico matalente zikwi zitatu za golidi, golidi wa Ofiri; ndi matalente zikwi zisanu ndi ziwiri a siliva woyengetsa, kumamatiza nazo makoma a nyumbazi;
5 golidi wa zija zagolidi, ndi siliva wa zija zasiliva, ndi za nchito ziri zonse akuzipanga manja a amisiri. Ndani uyo afuna mwini kudzipatulira kwa Yehova lero line?
6 Pamenepo akuru a nyumba za makolo, ndi akuru a mafuko a Israyeli, ndi akuru a zikwi ndi a mazana pamodzi ndi iwo oyang'anira nchito ya mfumu, anapereka mwaufulu,
7 napereka ku utumiki wa nyumba ya Mulungu golidi matalente zikwi zisanu, ndi madariki zikwi khumi; ndi siliva matalente zikwi khumi, ndi mkuwa matalente zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ndi citsulo matalente zikwi zana limodzi.
8 Ndipo amene anali nayo miyala ya mtengo wace anaipereka ku cuma ca nyumba ya Yehova, mwa dzanja la Yehieli Mgerisoni.
9 Ndipo anthu anakondwera popeza anapereka mwaufulu; pakuti ndi mtima wangwiro anapereka mwaufulu kwa Yehova; mfumu Davide yemwe anakondwera ndi cimwemwe cacikuru.