6 Pamenepo akuru a nyumba za makolo, ndi akuru a mafuko a Israyeli, ndi akuru a zikwi ndi a mazana pamodzi ndi iwo oyang'anira nchito ya mfumu, anapereka mwaufulu,
7 napereka ku utumiki wa nyumba ya Mulungu golidi matalente zikwi zisanu, ndi madariki zikwi khumi; ndi siliva matalente zikwi khumi, ndi mkuwa matalente zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ndi citsulo matalente zikwi zana limodzi.
8 Ndipo amene anali nayo miyala ya mtengo wace anaipereka ku cuma ca nyumba ya Yehova, mwa dzanja la Yehieli Mgerisoni.
9 Ndipo anthu anakondwera popeza anapereka mwaufulu; pakuti ndi mtima wangwiro anapereka mwaufulu kwa Yehova; mfumu Davide yemwe anakondwera ndi cimwemwe cacikuru.
10 Motero Davide analemekeza Yehova pamaso pa khamu lonse, nati Davide, Wolemekezedwa Inu, Yehova Mulungu wa Israyeli, Atate wathu ku nthawi zomka muyaya.
11 Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi kulakika, ndi cifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam'mwamba ndi pa dziko lap ansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse.
12 Zolemera ndi ulemu zifuma kwanu, ndipo mucita ufumu pa zonse, ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yaikuru; kukuza ndi kupatsa onse mphamvu kuli m'dzanja lanu.