2 Ndipo Samueli anati, Ndikamuka bwanji? Sauli akacimva, adzandipha. Ndipo Yehova anati, Umuke nayo ng'ombe yaikazi, nunene kuti, Ndadza kudzaphera nsembe kwa Yehova.
3 Ndipo uitane Jese abwere kunsembeko, ndipo Ine ndidzakusonyeza cimene uyenera kucita; ndipo udzandidzozera iye amene ndidzakuchulira dzina lace.
4 Ndipo Samueli anacita cimene Yehova ananena, nadza ku Betelehemu. Ndipo akuru a mudziwo anadza kukomana naye monthunthumira, nati, Mubwera ndi mtendere kodi?
5 Nati iye, Ndi mtendere umene; ndadza kudzaphera nsembe kwa Yehova; mudzipatule ndi kufika ndi ine kunsembeko. Ndipo iye anapatula Jese ndi ana ace, nawaitanira kunsembeko.
6 Ndipo kunali, pakufika iwo, iye anayang'ana pa Eliyabu, nati, Zoonadi, wodzozedwa wa Yehova ali pamaso pace.
7 Koma Yehova ananena ndi Samueli, Vsayang'ane nkhope yace, kapena kutalika kwa msinkhu wace, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana cooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima.
8 Pamenepo Jese anaitana Abinadabu nampititsa pa Samueli. Ndipo iye adati, Koma uyunso Yehova sadamsankha.