14 Ndipo ananena naye, Makhalidwe ace ndi otani? nati iye, Nkhalamba irikukwera yobvala mwinjiro. Pamenepo Sauli anazindikira kuti ndi Samueli, naweramitsa nkhope yace pansi, namgwadira.
15 Ndipo Samueli ananena ndi Sauli, Wandibvutiranji kundikweretsa kuno? Sauli nayankha, Ndirikusautsika kwambiri, pakuti Afilisti aponyana nkhondo ndi ine, ndipo Mulungu anandicokera, osandiyankhanso, kapena ndi aneneri, kapena ndi maloto; cifukwa cace ndakuitanani, kuti mundidziwitse cimene ndiyenera kucita.
16 Ndip'o Samueli ananena naye, Ndipo undifunsiranji ine, popeza Yehova anakucokera, nasandulika mdani wako?
17 Ndipo Yehova yekha wacita monga ananena pakamwa panga; ndipo Yehova wang'amba ufumuwo, kuucotsa m'dzanja lako, ndi kuupatsa mnansi wako, ndiye Davide.
18 Cifukwa sunamvera mau a Yehova, ndi kukwaniritsa mkwiyo wace woopsa pa Ameleki, cifukwa cace Yehova wakucitira cinthu ici lero.
19 Ndiponso Yehova adzapereka Israyeli pamodzi ndi iwe m'dzanja la Afilisti; ndipo mawa iwe ndi ana ako mudzakhala kuli ine; Yehova adzaperekanso khamu la Aisrayeli m'dzanja la Afilisti.
20 Pomwepo Sauli anagwa pansi tantha, naopa kwakukuru, cifukwa ca mau a Samueli; ndipo analibe mphamvu; pakuti tsiku lonse ndi usiku wace wonse anakhala osadya kanthu.