8 Ndipo Sauli anadzizimbaitsa nabvala zobvala zina, nanka iye pamodzi ndi anthu ena awiri, nafika kwa mkaziyo usiku; nati iye, Undilotere ndi mzimu wobwebwetawo, nundiukitsire ali yense ndidzakuchulira dzina lace.
9 Ndipo mkaziyo ananena naye, Onani, mudziwa cimene anacita Sauli, kuti analikha m'dzikomo obwebweta onse, ndi aula; cifukwa ninji tsono mulikuchera moyo wanga msampha, kundifetsa.
10 Ndipo Sauli anamlumbirira kwa Yehova, nati, Pali Yehova, palibe cilango cidzakugwera cifukwa ca cinthu ici.
11 Pomwepo mkaziyo anati, Ndikuukitsireni yani? Nati iye, Undiukitsire Samueli.
12 Ndipo mkaziyo pakuona Samueli, anapfuula ndi mau akuru; ndi mkaziyo analankhula ndi Sauli, nati, Munandinyengeranji? popeza inu ndinu Sauli.
13 Ndipo mfumuvo inanena naye, Usaope, kodi ulikuona ciani? Mkaziyo nanena ndi Sauli, Ndirikuona milungu irikukwera kuturuka m'kati mwa dziko.
14 Ndipo ananena naye, Makhalidwe ace ndi otani? nati iye, Nkhalamba irikukwera yobvala mwinjiro. Pamenepo Sauli anazindikira kuti ndi Samueli, naweramitsa nkhope yace pansi, namgwadira.