6 Koma ananena naye, Onatu, m'mudzi muno muli munthu wa Mulungu, ndiye munthu anthu amcitira ulemu; zonse azinena zicitika ndithu; tiyeni tipite komweko, kapena adzakhoza kutidziwitsa zimene tirikuyendera.
7 Ndipo Sauli ananena ndi mnyamata wace, Koma taona, tikapitako nmtengere ciani munthuyo? popeza mkate udatha m'zotengera zathu, ndiponso tiribe mphatso yakumtengera munthu wa Mulungu, tiri naco ciani?
8 Ndipo mnyamatayo anayankhanso kwa Sauli nati, Onani m'dzanja langa muli limodzi la magawo anai a sekeli wa siliva; ndidzampatsa munthu wa Mulungu limeneli kuti atiuze njira yathu.
9 Kale m'Israyeli, munthu akati afunse kwa Mulungu, adafotero kuti, Tiyeni tipite kwa mlauliyo; popeza iye wochedwa mneneri makono ano, anachedwa mlauli kale.
10 Pamenepo Sauli anati kwa mnyamata wace, Wanena bwino; tiye tipite. Comweco iwowa anapita kumudzi kumene kunali munthu wa Mulunguyo.
11 Pakukwera kumudziko anapeza anthu akazi alikuturuka kuti akatunge madzi, nanena nao, Mlauliyo alipo kodi?
12 Ndipo anawayankha nati, Alipo; onani ali m'tsogolo mwanu; fulumirani pakuti wabwera lero kumudzi kuno; popeza lero anthu akuti aphere nsembe pamsanje;