1 NDIPO Solomo mwana wa Davide analimbikitsidwa m'ufumu wace, ndipo Yehova Mulungu wace anali naye, namkuza kwakukuru.
2 Ndipo Solomo analankhula ndi Aisrayeli onse, ndi akuru a zikwi ndi a mazana, ndi kwa oweruza, ndi kwa kalonga ali yense wa Israyeli, akuru a nyumba za makolo.
3 Ndipo Solomo ndi khamu lonse pamodzi naye anamuka ku msanje wa ku Gibeoni; pakuti kumeneko kunali cihema cokomanako ca Mulungu adacimanga Mose mtumiki wa Yehova m'cipululu.
4 Koma likasa la Mulungu Davide adakwera nalo kucokera ku Kiriyati Yearimu kumka kumene Davide adalikonzeratu malo; pakuti adaliutsiratu hema ku Yerusalemu.
5 Guwa la nsembe lomwe lamkuwa, adalipanga Bezaleli mwana wa Uri mwana wa Huri linali komweko, ku khomo la kacisi wa Yehova; ndipo Solomo ndi khamulo anafunako.
6 Nakwerako Solomo ku guwa la nsembe pamaso pa Yehova linali ku cihema cokomanako, napereka pamenepo nsembe zopsereza cikwi cimodzi.