6 Nakwerako Solomo ku guwa la nsembe pamaso pa Yehova linali ku cihema cokomanako, napereka pamenepo nsembe zopsereza cikwi cimodzi.
7 Usiku womwewo Mulungu anaonekera kwa Solomo, nati kwa iye, Pempha comwe ndikupatse.
8 Nati Solomo kwa Mulungu, Mwacitira Davide atate wanga zokoma zambiri, ndipo mwandiika mfumu m'malo mwace.
9 Tsopano, Yehova Mulungu, likhazikike lonjezano lanu la kwa Davide atate wanga; pakuti mwandiika mfumu ya anthu akucuruka ngati pfumbi lapansi.
10 Mundipatse tsono nzeru ndi cidziwitso, kuti ndituruke ndi kulowa pamaso pa anthu awa; pakuti angathe ndani kuweruza anthu anu awa ambiri?
11 Ndipo Mulungu anati kwa Solomo, Popeza cinali mumtima mwako ici, osapempha cuma, akatundu, kapena ulemu, kapena moyo wa iwo akudana nawe, osapemphanso masiku ambiri; koma wadzipemphera nzeru ndi cidziwitso, kuti uweruze anthu anga amene ndakuika ukhale mfumu yao,
12 nzeru ndi cidziwitso zipatsidwa kwa iwe, ndidzakupatsanso cuma, ndi akatundu, ndi ulemu, zotere zonga sanakhala nazo mafumu akale usanakhale iwe, ndi akudza pambuyo pako sadzakhala nazo zotero.