1 Ndipo atafika ku Yerusalemu Rehabiamu, anamemeza a nyumba ya Yuda ndi Benjamini amuna osankhika zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu, ndiwo ankhondo, alimbane ndi Aisrayeli kubwezanso ufumu kwa Rehabiamu.
2 Koma mau a Yehova anadza kwa Semaya munthu wa Mulunguyo, ndi kuti,
3 Lankhula ndi Rehabiamu mwana wa Solomo mfumu ya Yuda ndi Benjamini, ndi kuti,
4 Atero Yehova, Musamuka kukayambana ndi abale anu, bwererani yense ku nyumba yace; pakuti cinthu ici cifuma kwa Ine. Ndipo anamvera mau a Yehova, nabwerera osakayambana ndi Yerobiamu.
5 Ndipo Rehabiamu anakhala m'Yerusalemu, namanga midzi yolimbikiramo m'Yuda.
6 Anamangadi Betelehemu, ndi Etamu, ndi Tekoa,
7 ndi Betezuri, ndi Soko, ndi Adulamu,