2 Naika ankhondo m'midzi yonse yamalinga ya Yuda, naika aboma m'dziko la Yuda, ndi m'midzi ya Efraimu, imene adailanda Asa atate wace.
3 Ndipo Yehova anali ndi Yehosafati, popeza anayenda m'njira zace zoyamba za kholo lace Davide, osafuna Abaala;
4 koma anafuna Mulungu wa kholo lace nayenda m'malamulo ace, osatsata macitidwe a Israyeli.
5 Cifukwa cace Yehova anakhazikitsa ufumuwo m'dzanja lace, ndi onse Ayuda anabwera nayo mitulo kwa Yehosafati; ndipo zidamcurukira cuma ndi ulemu.
6 Ndi mtima wace unakwezeka m'njira za Yehova; anacotsanso misanje ndi zifanizo m'Yuda.
7 Caka cacitatu ca ufumu wace anatuma akalonga ace, ndiwo Benihayili, ndi Obadiya, ndi Zekariya, ndi Netaneli, ndi Mikaya, aphunzitse m'midzi ya Yuda;
8 ndi pamodzi nao Alevi, ndiwo Semaya, ndi Netaniya, ndi Zebadiya, ndi Asaheli, ndi Semiramoti, ndi Yonatani, ndi Adoniya, ndi Tobiya, ndi Tobadoniya, Alevi; ndi pamodzi nao Elisama ndi Yoramu, ansembe.